Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 34:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Samalani, kuopera kuti mungachite pangano ndi anthu okhala m’dzikomo, pakuti iwo adzachita chiwerewere ndi milungu yawo+ ndi kupereka nsembe kwa milungu yawo.+ Chifukwa mukachita nawo pangano, mosakayikira wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+

  • Oweruza 2:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ana a Isiraeli sanamvere ngakhale oweruza awo, koma anachita chiwerewere+ ndi milungu ina+ ndi kuigwadira. Iwo anapatuka mwamsanga panjira imene makolo awo anayendamo. Makolo awo anayenda m’njira imeneyo mwa kumvera malamulo a Yehova,+ koma iwo sanachite mofanana ndi makolo awo.

  • Salimo 106:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Anali kupereka nsembe ana awo aamuna+

      Ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.+

  • Salimo 106:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo,+

      Zochita zawo zinawalowetsa m’makhalidwe oipa.+

  • Yeremiya 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pali mawu akuti: “Mwamuna akathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo n’kuchokadi ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, sangabwererenso kwa mwamuna woyamba uja.”+

      Kodi dzikoli silinaipitsidwe kale?+

      Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+ Kodi m’poyenera kuti ubwererenso kwa ine?+

  • Ezekieli 16:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “‘Koma unayamba kudalira kukongola kwako+ ndipo unakhala hule chifukwa cha kutchuka kwa dzina lako.+ Unayamba kuchita uhule mosadziletsa ndi munthu aliyense wodutsa m’njira.+ Kukongola kwako unakupereka kwa anthu odutsawo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena