15 Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+