Ekisodo 14:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+ Nehemiya 9:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+ Salimo 78:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,+Ndipo anaimitsa madzi kukhala ngati khoma.+ Yesaya 43:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Izi n’zimene Yehova wanena, yemwe amapanga njira panyanja. Amapanga msewu ngakhale pamadzi amphamvu.+ Yesaya 63:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ali kuti amene anachititsa mkono wake wokongola+ kupita kudzanja lamanja la Mose, amene anagawanitsa madzi pamaso pawo+ kuti adzipangire dzina lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+ Aheberi 11:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Mwa chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka Nyanja Yofiira ngati kuti akudutsa pamtunda pouma,+ koma Aiguputo atalimba mtima ndi kulowa panyanjapo, nyanjayo inawamiza.+
21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+
11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+
16 Izi n’zimene Yehova wanena, yemwe amapanga njira panyanja. Amapanga msewu ngakhale pamadzi amphamvu.+
12 Ali kuti amene anachititsa mkono wake wokongola+ kupita kudzanja lamanja la Mose, amene anagawanitsa madzi pamaso pawo+ kuti adzipangire dzina lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+
29 Mwa chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka Nyanja Yofiira ngati kuti akudutsa pamtunda pouma,+ koma Aiguputo atalimba mtima ndi kulowa panyanjapo, nyanjayo inawamiza.+