Masalimo
2 Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mwambi.+
Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale,+
3 Amene tinamva ndipo tikuwadziwa,+
Komanso amene makolo athu anatifotokozera.+
4 Mbadwa zawo sitikuzibisira mawu ophiphiritsawa,+
Ndipo tidzawasimba ngakhale ku mibadwo ya m’tsogolo.+
Tidzasimba ntchito zotamandika za Yehova ndi mphamvu zake,+
Komanso zinthu zodabwitsa zimene wachita.+
5 Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,+
Iye anaika chilamulo mu Isiraeli,+
Zinthu zimene analamula makolo athu,+
Kuti auze ana awo.+
6 Kuti m’badwo wa m’tsogolo, ana amene adzabadwe m’tsogolo, adzadziwe zimenezi,+
Kuti nawonso adzanyamuke ndi kusimbira ana awo.+
7 Kuti anawo azidzadalira Mulungu,+
Ndi kuti asadzaiwale zochita za Mulungu+ koma kuti azidzasunga malamulo ake.+
8 Ndipo asadzakhale ngati makolo awo,+
M’badwo wosamva ndi wopanduka,+
M’badwo umene sunakonze mtima wawo,+
Ndipo maganizo awo sanali okhulupirika kwa Mulungu.+
14 Iye anapitiriza kuwatsogolera ndi mtambo masana,+
Ndipo usiku wonse anali kuwatsogolera ndi kuwala kwa moto.+
17 Koma iwo anapitiriza kumuchimwira+
Mwa kupandukira Wam’mwambamwamba m’dera lopanda madzi.+
18 Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu m’mitima yawo+
Mwa kupempha chakudya china chimene mtima wawo unalakalaka.+
19 Pamenepo anayamba kulankhula mawu oipa kwa Mulungu.+
Iwo anati: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya m’chipululu muno?”+
20 Taonani! Kodi Mulungu si uja anamenya thanthwe+
Kuti madzi atuluke, kutinso patuluke mitsinje yodzaza madzi?+
Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,+
Kapena kodi angakonzere anthu ake chakudya?”+
21 Choncho Yehova anamva zimenezo ndipo anakwiya.+
Moti moto unayakira Yakobo,+
Ndipo mkwiyo unatsikira pa Isiraeli.+
24 Ndipo anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.+
Iye anawapatsa tirigu wochokera kumwamba.+
26 Anachititsa mphepo ya kum’mawa kuwomba m’mlengalenga,+
Ndipo mwa mphamvu zake anachititsa mphepo ya kum’mwera kuwomba.+
27 Iye anagwetsa chakudya pa iwo ngati fumbi.+
Anawagwetsera zolengedwa zamapiko zouluka, zochuluka ngati mchenga wakunyanja.+
30 Iwo anafunabe chakudya china,
Pamene china chinali m’kamwa.+
31 Nthawi yomweyo, mkwiyo wa Mulungu unatsikira pa iwo.+
Iye anayamba kupha anthu awo amphamvu.+
Ndipo anakomola anyamata a mu Isiraeli.
32 Ngakhale zinali choncho, iwo anawonjezera machimo awo,+
Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa.+
33 Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+
Anadula zaka za moyo wawo ndi masoka.
34 Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo anali kumufunafuna.+
Anali kutembenuka ndi kuyamba kufunafuna Mulungu.+
35 Iwo anali kukumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,+
Ndiponso kuti Mulungu Wam’mwambamwamba anali Wowabwezerera.+
36 Koma iwo anali kufuna kum’pusitsa ndi pakamwa pawo.+
Ndi lilime lawo anali kufuna kunena bodza kwa iye.+
38 Koma anawamvera chifundo.+ Anali kukhululukira* machimo awo+ ndipo sanali kuwawononga.+
Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake,+
Ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.
39 Iye anali kukumbukira nthawi zonse kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+
Anali kukumbukira kuti moyo wawo umachoka ndipo subwereranso.+
42 Iwo sanakumbukire dzanja la Mulungu,+
Sanakumbukire tsiku limene anawawombola kwa mdani wawo,+
43 Iwo sanakumbukire mmene anaikira zizindikiro zake mu Iguputo,+
Ndi zozizwitsa zimene anachita m’dera la Zowani,+
44 Mmene anasinthira mitsinje ing’onoing’ono yotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,+
Moti sanathe kumwa madzi ake.+
49 Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,+
Ukali, ziweruzo zamphamvu ndi masautso.+
Anawatumizira makamu a angelo obweretsa masoka.+
51 Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa mu Iguputo,+
Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka m’mahema a Hamu.+
52 Kenako anachititsa anthu ake kuchoka m’dzikolo ngati gulu la nkhosa,+
Anawayendetsa m’chipululu ngati gulu la ziweto.+
54 Kenako anawalowetsa m’dziko lake lopatulika,+
M’dera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+
55 Chifukwa cha iwo anachotsa mitundu ina pang’onopang’ono m’dzikoli,+
Ndipo anayesa dzikoli ndi kuligawa kwa iwo kukhala cholowa chawo,+
Moti anachititsa mafuko a Isiraeli kukhala m’nyumba zawozawo.+
56 Koma iwo anayamba kuyesa Mulungu Wam’mwambamwamba ndi kum’pandukira,+
Ndipo sanasunge zikumbutso zake.+
57 Iwo anali kubwerera ndi kuchita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.+
Anapotoka maganizo ngati uta wosakunga kwambiri.+
58 Iwo anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+
Ndipo anamuchititsa nsanje ndi zifaniziro zawo zogoba.+
60 Pamapeto pake anasiya chihema chopatulika cha ku Silo,+
Hema limene anali kukhalamo pakati pa anthu ochokera kufumbi.+
61 Analola kuti chizindikiro cha mphamvu zake chitengedwe ndi adani ake,+
Iye analola kuti chizindikiro cha kukongola kwake chikhale m’manja mwa adani.+
65 Pamenepo Yehova anagalamuka ngati akudzuka kutulo,+
Ngati munthu wamphamvu amene akugalamuka pambuyo pomwa vinyo wambiri.+
69 Anayamba kumanga malo opatulika ngati malo okwera a paphiri,+
Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+