Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma ndakusiya ndi moyo+ kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+

  • Deuteronomo 28:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pamenepo mitundu yonse ya anthu padziko lapansi adzaona kuti mukutchedwa ndi dzina la Yehova,+ ndipo adzachita nanu mantha.+

  • 1 Samueli 17:46
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 46 Lero Yehova akupereka m’manja mwanga,+ ndipo ndikupha ndi kukudula mutu. Lero ndipereka mitembo ya anthu a m’misasa ya Afilisiti kwa mbalame zam’mlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire.+ Anthu onse a padziko lapansi adzadziwa kuti Isiraeli ali ndi Mulungu.+

  • 1 Mafumu 8:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 (popeza adzamva za dzina lanu lalikulu,+ za dzanja lanu lamphamvu+ ndi mkono wanu wotambasuka), ndipo wabwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino,+

  • 2 Mafumu 5:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kenako iye pamodzi ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona+ uja. Anaima pamaso pake n’kunena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti, padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu kupatula ku Isiraeli kokha.+ Ndiye landirani mphatso+ kuchokera kwa ine mtumiki wanu.”

  • 2 Mafumu 19:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ chonde tipulumutseni+ m’manja mwake, kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena