Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 11:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yoswa analanda dziko lonselo, dera lamapiri, dera lonse la Negebu,+ dziko lonse la Goseni,+ ku Sefela,+ ku Araba+ ndiponso dera lamapiri la Isiraeli ndi zigwa zake.+

  • Yoswa 21:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Kuwonjezera apo, Yehova anawapatsa mpumulo+ pakati pa adani awo onse owazungulira, mogwirizana ndi zonse zimene analumbirira+ makolo awo. Panalibe ngakhale mdani mmodzi pa adani awo onse amene anatha kulimbana nawo.+ Yehova anapereka adani awo onse m’manja mwawo.+

  • Nehemiya 9:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Choncho ana awo+ analowa ndi kutenga dzikolo,+ ndipo munagonjetsa+ anthu okhala m’dzikolo, Akanani,+ ndi kuwapereka m’manja mwawo. Munaperekanso ngakhale mafumu a Akananiwo+ ndi mitundu ya anthu ya m’dzikolo+ kwa ana a Isiraeliwo kuti awachite zimene akufuna.+

  • Salimo 78:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 Chifukwa cha iwo anachotsa mitundu ina pang’onopang’ono m’dzikoli,+

      Ndipo anayesa dzikoli ndi kuligawa kwa iwo kukhala cholowa chawo,+

      Moti anachititsa mafuko a Isiraeli kukhala m’nyumba zawozawo.+

  • Salimo 105:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Pang’onopang’ono anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,+

      Ndipo zipatso za ntchito imene mitundu ya anthu inagwira mwakhama, anazitenga kukhala zawo,+

  • Machitidwe 7:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Ndipo makolo athu amene anachilandira kwa makolo awo, analowa nacho limodzi ndi Yoswa,+ m’dziko limene linali m’manja mwa anthu a mitundu ina+ amene Mulungu anawapitikitsa pamaso pa makolo athu.+ Chihemacho chinakhala m’dziko limeneli mpaka m’masiku a Davide.

  • Machitidwe 13:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndipo atawononga mitundu 7 m’dziko la Kanani, anagawa dzikolo kwa Aisiraeli mwa kuchita maere.+

  • Aheberi 11:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Mwa chikhulupiriro, makoma a Yeriko anagwa, atawazungulira masiku 7.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena