Genesis 17:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Muzichita mdulidwe kuti ukhale chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi inu.+ Ekisodo 4:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Zitatero, Zipora+ anatenga mwala wakuthwa n’kudula khungu+ la mwana wakeyo. Ndipo khungu analidulalo analiponya pamapazi ake n’kunena kuti: “Popeza ndinu mkwati wa magazi kwa ine.”
25 Zitatero, Zipora+ anatenga mwala wakuthwa n’kudula khungu+ la mwana wakeyo. Ndipo khungu analidulalo analiponya pamapazi ake n’kunena kuti: “Popeza ndinu mkwati wa magazi kwa ine.”