Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+

      Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala chete ngati mwala.

      Kufikira anthu anu+ atadutsa, inu Yehova,

      Kufikira anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+

  • Deuteronomo 2:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Lero ndichititsa anthu a mitundu ina okhala pansi pa thambo, amene adzamva za inu, kuchita nanu mantha kwambiri ndi kuyamba kukuopani. Chifukwa cha inu, iwo adzanthunthumira ndi kumva zopweteka zofanana ndi zowawa za pobereka.’+

  • Deuteronomo 11:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Palibe munthu amene adzaima kuti alimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzapondapo kugwidwa ndi mantha aakulu ndi kukuopani,+ monga mmene anakulonjezerani.

  • Yoswa 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Titangomva zimenezi, mitima yathu inayamba kusungunuka ndi mantha,+ ndipo mpaka pano palibe aliyense amene akulimba mtima, chifukwa choopa inu.+ Ndithu, Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa kumwamba ndi padziko lapansi.+

  • Yoswa 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali m’mphepete mwa nyanja, anamva zakuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pa ana a Isiraeli kufikira atawoloka. Atamva zimenezo, mitima yawo inasungunuka ndi mantha,+ moti anatheratu mphamvu poopa ana a Isiraeli.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena