13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa m’dera la chigwa cha Arinoni,+ m’chipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori.
9 Cholowa chawo chinayambira kumzinda wa Aroweli+ umene uli m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni,+ ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho, kuphatikizapo malo onse okwererapo a Medeba+ mpaka kukafika ku Diboni.+