35 “‘Limeneli ndilo linali gawo la Aroni monga wansembe ndiponso gawo la ana ake monga ansembe. Gawoli linali lochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, malinga ndi zimene anawalamula pa tsiku limene anaperekedwa+ kuti atumikire monga ansembe a Yehova.