Genesis 18:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Popeza mwadzera njira yodutsa kwa kapolo wanu, mundilole ndikukonzereni kachakudya kuti mutsitsimutse mitima yanu.+ Mukatero mukhoza kupitiriza ulendo wanu.” Pamenepo iwo anati: “Chabwino, chita mmene waneneramo.” Oweruza 19:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pa tsiku lachinayi, atadzuka m’mawa kwambiri monga mwa nthawi zonse, anakonzeka kuti anyamuke, koma bambo a mtsikanayo anauza mkamwini wawoyo kuti: “Yambani mwadya kaye mkate,+ kenako mukhoza kupita.” Rute 3:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Boazi anadya ndi kumwa, ndipo anali wosangalala mumtima mwake.+ Kenako anapita kukagona chakumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndi kuvundukula kumapazi kwa Boazi n’kugona. Salimo 104:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+
5 Popeza mwadzera njira yodutsa kwa kapolo wanu, mundilole ndikukonzereni kachakudya kuti mutsitsimutse mitima yanu.+ Mukatero mukhoza kupitiriza ulendo wanu.” Pamenepo iwo anati: “Chabwino, chita mmene waneneramo.”
5 Pa tsiku lachinayi, atadzuka m’mawa kwambiri monga mwa nthawi zonse, anakonzeka kuti anyamuke, koma bambo a mtsikanayo anauza mkamwini wawoyo kuti: “Yambani mwadya kaye mkate,+ kenako mukhoza kupita.”
7 Boazi anadya ndi kumwa, ndipo anali wosangalala mumtima mwake.+ Kenako anapita kukagona chakumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndi kuvundukula kumapazi kwa Boazi n’kugona.
15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+