3 Zitatero, mwamuna wakeyo ananyamuka kukakambirana naye mofatsa kuti abwerere. Pa ulendowo anali limodzi ndi mtumiki wake+ ndi abulu awiri. Atafika kumeneko, mkaziyo analowetsa mwamuna wakeyo m’nyumba ya bambo ake ndipo iwo atamuona anasangalala kwambiri kukumana naye.