22 Ndiyeno asilikali amene analanda mzinda aja anatuluka mumzindamo kudzamenyana ndi amuna a ku Aiwo. Chotero amuna a ku Ai anakhala pakati pa Aisiraeli, ena mbali iyi, ena mbali inayo. Pamenepo Aisiraeli anapha amuna a ku Ai, moti panalibe wotsala ndi moyo kapena wothawa.+