19 Atafika pamiyala yogoba imene inali ku Giligala,+ anabwerera kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “Pepanitu mfumu, ndili ndi uthenga wachinsinsi woti ndikuuzeni.” Pamenepo mfumuyo inati: “Khala chete!” Itatero, onse amene anaimirira pafupi ndi mfumuyo anatuluka.+