Levitiko 9:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ n’kunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi, anayamba kufuula mokondwera+ ndipo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi. Oweruza 13:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Pamene lawi la moto linali kukwera m’mwamba kuchokera paguwalo, mngelo wa Yehova nayenso anakwera kumwamba m’lawi la moto wa paguwa lansembelo, Manowa ndi mkazi wake akuonerera.+ Nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 1 Mafumu 18:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Atatero, moto+ wa Yehova unatsika n’kunyeketsa nsembe yopsereza+ ija, nkhuni, miyala ndi fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali m’ngalande muja.+ 1 Mbiri 21:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Ndiyeno Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamalopo,+ ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Komanso anaitana pa dzina la Yehova+ yemwe tsopano anamuyankha ndi moto+ wochokera kumwamba umene unafika paguwa lansembe yopsereza. 2 Mbiri 7:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Tsopano Solomo atangomaliza kupemphera,+ moto unatsika kuchokera kumwamba.+ Motowo unanyeketsa nsembe yopsereza+ pamodzi ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova+ unadzaza nyumbayo.
24 ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ n’kunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi, anayamba kufuula mokondwera+ ndipo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.
20 Pamene lawi la moto linali kukwera m’mwamba kuchokera paguwalo, mngelo wa Yehova nayenso anakwera kumwamba m’lawi la moto wa paguwa lansembelo, Manowa ndi mkazi wake akuonerera.+ Nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
38 Atatero, moto+ wa Yehova unatsika n’kunyeketsa nsembe yopsereza+ ija, nkhuni, miyala ndi fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali m’ngalande muja.+
26 Ndiyeno Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamalopo,+ ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Komanso anaitana pa dzina la Yehova+ yemwe tsopano anamuyankha ndi moto+ wochokera kumwamba umene unafika paguwa lansembe yopsereza.
7 Tsopano Solomo atangomaliza kupemphera,+ moto unatsika kuchokera kumwamba.+ Motowo unanyeketsa nsembe yopsereza+ pamodzi ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova+ unadzaza nyumbayo.