6 Kenako mkaziyo anapita kukauza mwamuna wake kuti: “Munthu wa Mulungu woona anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ofanana ndi mngelo wa Mulungu woona,+ maonekedwe ochititsa mantha kwambiri.+ Koma sindinam’funse kumene wachokera ndiponso sanandiuze dzina lake.+