12 Ng’ombezo zinayamba kuyenda, kulunjika msewu wa ku Beti-semesi.+ Zinali kuyenda pamsewu waukulu wopita kumeneko zikulira, ndipo sizinapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. Apa n’kuti olamulira ogwirizana+ a Afilisiti akuzitsatira pambuyo mpaka kukafika m’malire a Beti-semesi.