Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 18:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ndipo Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli yense ndi kuwapatsa udindo wokhala atsogoleri a anthu,+ kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.

  • Oweruza 21:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndiyeno akulu a khamulo ananena kuti: “Tsopano popeza kuti akazi awonongedwa m’fuko la Benjamini, tichita chiyani ndi amuna amene atsala opanda akaziwa?”

  • 1 Samueli 4:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndiyeno anthuwo atabwerera kumsasa, akulu a Isiraeli anayamba kunena kuti: “N’chifukwa chiyani lero Yehova watigonjetsa pamaso pa Afilisiti?+ Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova+ ku Silo, kuti likhale pakati pathu ndi kutipulumutsa m’manja mwa adani athu.”

  • 2 Samueli 5:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Choncho akulu onse+ a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Mfumu Davide anachita nawo pangano+ ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli.+

  • 1 Mafumu 20:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Mfumu ya Isiraeli itamva mawu amenewa, inaitanitsa akulu onse a m’dzikolo+ n’kuwauza kuti: “Taonani, munthu uyu akufuna kutibweretsera tsoka.+ Ananditumizira uthenga woti akufuna akazi anga, ana anga aamuna, siliva wanga, ndi golide wanga, ndipo ine sindinamukanize ayi.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena