29 N’zosatheka kuti ife lero tipandukire Yehova+ mwadala, n’kuleka kutsatira Yehova mwa kumanga guwa lansembe loti tiziperekerapo nsembe zopsereza, zambewu ndi nsembe zina, kusiya guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, limene lili patsogolo pa chihema chake chopatulika!”+