11 Atafika pamalo otsetsereka otchedwa Beti-horoni pothawa Aisiraeli, Yehova anawagwetsera miyala ikuluikulu ya matalala+ kuchokera kumwamba yomwe inawagwera ndi kuwapha mpaka kukafika ku Azeka. Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambiri kuposa amene ana a Isiraeli anapha ndi lupanga.
13 Malirewo anapitirira kukafika ku Luzi,+ kutanthauza Beteli.+ Anakafika kum’mwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, n’kutsetserekera ku Ataroti-adara,+ n’kukadutsa paphiri la kum’mwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+