18 Pamenepo amuna atatu aja anakalowa mwamphamvu mumsasa wa Afilisiti, n’kutunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chinali pachipata. Atatero ananyamula madziwo n’kupita nawo kwa Davide.+ Koma Davide anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.+