26 Ndalamazo udzagulire chilichonse chimene mtima wako wakhumba,+ kaya ndi ng’ombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa+ ndi chilichonse chimene mtima wako wafuna. Ndipo uzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wako ndi kukondwera,+ iweyo ndi banja lako.