2 Panali amuna awiri, atsogoleri a magulu a achifwamba+ a mwana wa Sauli. Mmodzi dzina lake anali Bana ndipo wina dzina lake anali Rekabu. Onsewa anali ana a Rimoni Mbeeroti+ wa fuko la Benjamini, pakuti dera la Beeroti nalonso linali kuonedwa ngati gawo la fuko la Benjamini.