4 Komanso kuti Yehova adzakwaniritse mawu ake okhudza ine amene analankhula,+ akuti, ‘Ana ako+ akadzasamalira njira zawo, mwa kuyenda+ mokhulupirika*+ pamaso panga ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+
11 ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+