5 Tsopano mneneri Semaya+ anapita kwa Rehobowamu ndi kwa akalonga a Yuda amene anasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisaki. Iye anawauza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Inuyo mwandisiya,+ choncho inenso ndakusiyani+ ndipo ndakuperekani m’manja mwa Sisaki.’”