Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mlaliki 5:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo+ zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo.+ Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo+ akuona,+ ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.

  • Mlaliki 8:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pali chinthu china chachabe chimene chimachitika padziko lapansi: Pali anthu olungama amene amakumana ndi zinthu zimene amayenera kukumana nazo anthu oipa,+ ndiponso pali anthu oipa amene amakumana ndi zinthu zimene amayenera kukumana nazo anthu olungama.+ Ndinanena kuti zimenezinso n’zachabechabe.

  • Habakuku 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Inu ndinu woyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa ndipo simungathe kuonerera khalidwe loipa.+ N’chifukwa chiyani mumayang’ana anthu amene amachita zachinyengo,+ ndipo n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala chete pamene munthu woipa akumeza munthu amene ndi wolungama kuposa iyeyo?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena