Mlaliki
5 Samala mayendedwe+ ako ukapita kunyumba ya Mulungu woona. Ukapita kumeneko uzikamvetsera,+ osati uzikapereka nsembe monga mmene amachitira anthu opusa,+ pakuti iwo sadziwa kuti akuchita zoipa.+
2 Usamapupulume kulankhula, ndipo mtima wako+ usamafulumire kulankhula pamaso pa Mulungu woona,+ chifukwa Mulungu woona ali kumwamba+ koma iwe uli padziko lapansi. N’chifukwa chake suyenera kulankhula zambiri.+ 3 Pakuti maloto amabwera chifukwa chochuluka zochita,+ ndipo kuchuluka kwa mawu kumachititsa munthu kulankhula zinthu zopusa.+ 4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+ 5 Kuli bwino kuti usalonjeze+ kusiyana ndi kulonjeza koma osakwaniritsa zimene walonjezazo.+ 6 Usalole kuti pakamwa pako pakuchimwitse,+ komanso usamanene kwa mngelo+ kuti unalakwitsa.+ Kodi Mulungu woona akwiyirenji chifukwa cha mawu ako n’kuwononga ntchito ya manja ako?+ 7 Chifukwa chochuluka zochita pamakhala maloto,+ zinthu zachabechabe, ndi mawu ochuluka. Koma uziopa Mulungu woona yekha.+
8 Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo+ zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo.+ Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo+ akuona,+ ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.
9 Komanso, phindu la dziko lapansi ndi la munthu aliyense,+ chifukwa ngakhale mfumu imadalira kuti munda wake ulimidwe, kuti ipindule ndi zokolola za kumundako.+
10 Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.+ Zimenezinso n’zachabechabe.+
11 Zinthu zabwino zikachuluka ozidya amachulukanso,+ ndipo kodi mwiniwake wa zinthuzo amapindula chiyani kuposa kumangoziyang’ana ndi maso ake?+
12 Wotumikira munthu wina amagona tulo tokoma+ ngakhale adye zochepa kapena zambiri. Koma zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.
13 Pali chinthu chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndaona padziko lapansi pano: Munthu kumangosunga chuma chake n’kudzapwetekedwa nacho.+ 14 Chumacho chimatha+ chifukwa cha zoipa zinazake zimene zachitika, kenako iye amabereka mwana wamwamuna pamene alibe chilichonse choti angapatse mwanayo ngati cholowa.+
15 Monga mmene munthu anabadwira kuchokera m’mimba mwa mayi ake, adzapitanso wamaliseche+ ngati mmene anabwerera, ndipo palibe chilichonse chimene adzatenge+ pa ntchito yake imene anaigwira mwakhama.
16 Palinso chinthu china chomvetsa chisoni kwambiri: Monga mmene munthu anabwerera, adzapitanso chimodzimodzi. Kodi pali phindu lanji kwa munthu amene amachita khama kugwirira ntchito mphepo?+ 17 Komanso, masiku onse a moyo wake amadya chakudya chake mu mdima ndi kusautsika mtima kwakukulu,+ amadwala, ndiponso amakhala ndi nkhawa.
18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso chokongola chimene ine ndaona, n’chakuti munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala, chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta+ imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku onse a moyo wake amene Mulungu woona wam’patsa. Pakuti imeneyo ndiyo mphoto yake. 19 Komanso, munthu aliyense amene Mulungu woona wam’patsa chuma ndiponso zinthu zambiri,+ ndiye kuti wamulola kuti adye kuchokera pa zinthuzo.+ Wamulolanso kuti alandire mphoto yake ndi kusangalala chifukwa cha ntchito yake imene amaigwira mwakhama.+ Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+ 20 Pakuti zowawa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukira kawirikawiri, chifukwa Mulungu woona akuchititsa kuti mtima wake uzisangalala.+