21 Tsopano wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo ndi lumbiro la temberero.+ Iye aziti kwa mkaziyo: “Yehova akuike kukhala chitsanzo cha temberero ndi lumbiroli pakati pa anthu amtundu wako. Yehova achite zimenezo mwa kufotetsa ntchafu*+ yako, ndi kutupitsa mimba yako.