-
1 Mafumu 14:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Yehova adzawonongadi Isiraeli, ndipo zidzakhala ngati mmene bango limagwedezekera m’madzi,+ ndiponso adzazuladi+ Aisiraeli, kuwachotsa padziko labwinoli+ limene anapatsa makolo awo. Ndiyeno adzawabalalitsira+ kutsidya lina la Mtsinje,*+ popeza iwo anapanga mizati yawo yopatulika,+ n’kukwiyitsa+ nayo Yehova.
-
-
Nehemiya 9:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Choncho iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire+ zochita zanu zodabwitsa zimene munawachitira, m’malomwake anaumitsa khosi lawo+ ndipo anasankha mtsogoleri+ kuti awatsogolere pobwerera ku ukapolo wawo ku Iguputo. Koma inu ndinu Mulungu wokhululuka,+ wachisomo+ ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha,+ chotero simunawasiye.+
-