30 Itatero, mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova+ limodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu okhala ku Yerusalemu, ansembe,+ Alevi, ndi anthu onse, wamng’ono ndi wamkulu yemwe. Tsopano mfumuyo inayamba kuwawerengera+ mawu onse a m’buku la pangano limene linapezeka panyumba ya Yehova.+