-
2 Mafumu 11:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala+ malinga ndi mwambo wawo. Anaonanso atsogoleri a asilikali ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba malipenga. Nthawi yomweyo Ataliya+ anang’amba zovala zake n’kuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+
-
-
2 Mbiri 23:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala chake+ pakhomo. Anaonanso akalonga+ ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba+ malipenga. Panalinso oimba+ ndi zipangizo zoimbira ndiponso anthu otsogolera poimba nyimbo zotamanda. Nthawi yomweyo Ataliya anang’amba zovala zake n’kuyamba kunena kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+
-