-
2 Mbiri 23:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala* pakhomo. Akalonga+ ndi anthu oimba malipenga anali limodzi ndi mfumuyo ndipo anthu onse amʼdzikolo ankasangalala+ komanso ankaimba malipenga. Panalinso oimba ndi zipangizo zoimbira amene ankatsogolera poimba nyimbo zotamanda. Ataliya ataona zimenezi anangʼamba zovala zake nʼkuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”
-