Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 25:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Awa ndi mawu amene Yeremiya anauzidwa onena za anthu onse a mu Yuda m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, chimenenso chinali chaka choyamba cha ulamuliro wa Nebukadirezara mfumu ya Babulo.

  • Yeremiya 46:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Uthenga umenewu unali wopita ku Iguputo+ ndipo unali kukhudza gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya Iguputo,+ amene anali kumtsinje wa Firate ku Karikemisi.+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo anagonjetsa mfumu imeneyi m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Uthengawo unali wakuti:

  • Danieli 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 M’chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu+ mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu ndipo anazungulira mzindawo.+

  • Danieli 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Nebukadinezara anapanga fano lagolide.+ Fanoli linali lalitali mikono* 60 ndipo m’lifupi mwake linali mikono 6. Analiimika m’chigwa cha Dura, m’chigawo cha Babulo.+

  • Danieli 4:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Nthawi yomweyo+ mawuwa anakwaniritsidwa pa Nebukadinezara ndipo anathamangitsidwa pakati pa anthu. Iye anayamba kudya udzu ngati ng’ombe ndipo thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba. Tsitsi lake linatalika kwambiri ngati nthenga za chiwombankhanga ndipo zikhadabo zake zinatalika ngati za mbalame.+

  • Danieli 4:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 “Tsopano ine Nebukadinezara ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba,+ chifukwa ntchito zake zonse ndizo choonadi, njira zake ndi zolungama,+ ndiponso amatha kutsitsa anthu onyada.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena