6 Choncho Yehu ananyamuka n’kulowa m’nyumba. Mmenemo mtumiki wa mneneri uja anatenga mafuta aja n’kumuthira pamutu. Kenako anamuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikukudzoza iwe kukhala mfumu+ ya anthu a Yehova,+ kutanthauza Aisiraeli.