4 Ukamuuze kuti, ‘Ganizira mofatsa zochita zako.+ Usatekeseke kapena kuchita mantha. Mtima wako usaope+ zikuni ziwiri zimene zikungofuka utsi, zomwe zatsala pang’ono kunyekeratu. Usaope mkwiyo waukulu wa Rezini mfumu ya Siriya ndiponso usaope mwana wa Remaliya,+