-
2 Mbiri 2:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 ine ndikumanga+ nyumba ya dzina+ la Yehova Mulungu wanga kuti ndiipatule+ ikhale yake. Ndikufuna kuti ndizifukiziramo mafuta onunkhira+ pamaso pake, ndi kuti nthawi zonse muzikhala mkate wosanjikiza.+ Ndiponso m’nyumbayo ndiziperekeramo nsembe zopsereza m’mawa ndi madzulo+ pa masabata,+ pa masiku okhala mwezi,+ ndi pa nyengo ya zikondwerero+ za Yehova Mulungu wathu. Zimenezi zizichitika mu Isiraeli mpaka kalekale.*+
-
-
2 Mbiri 31:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Kuchokera pa katundu wake,+ mfumuyo inapereka nsembe zopsereza za m’mawa+ ndi za madzulo, komanso nsembe zopsereza za masabata,+ za masiku okhala mwezi+ ndi za panyengo zochita chikondwerero,+ monga gawo limene inayenera kupereka la nsembe zopsereza,+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Yehova.+
-