32Tsopano ana a Rubeni+ ndi ana a Gadi+ anakhala ndi ziweto zambiri, zankhaninkhani. Iwo anayamba kusirira dziko la Yazeri+ ndi la Giliyadi, ndipo deralo linalidi malo abwino a ziweto.
10 Tinalanda mizinda yonse ya kudera lokwererapo, m’Giliyadi monse, m’Basana monse, mpaka ku Saleka+ ndi ku Edirei,+ mizinda ya m’dera la ufumu wa Ogi ku Basana.