30 Kumbali ya Aheburoni,+ panali Hasabiya ndi abale ake, amuna odalirika+ okwanira 1,700. Iwowa anali ndi ntchito yoyang’anira Aisiraeli m’chigawo cha Yorodano kumadzulo, pa ntchito zonse za Yehova ndiponso pa ntchito zotumikira mfumu.
7 Wansembe ayenera kuphunzitsa anthu kuti adziwe Mulungu. Anthuwo ayenera kufunafuna kumva chilamulo kuchokera pakamwa pake,+ pakuti iye ndi mthenga wa Yehova wa makamu.+