41 Anthu otchulidwa mayinawa anapita kumeneko m’masiku a Hezekiya+ mfumu ya Yuda n’kukagwetsa+ mahema a Ahamu, n’kupha Ameyuni amene anali kumeneko. Anawawononga+ anthuwo, ndipo iwo kulibe mpaka lero. Kenako iwo anayamba kukhala kumeneko m’malo mwawo, chifukwa kunali msipu+ wa ziweto zawo.