3 Ndiyeno wansembeyo aone nthenda imene yatuluka pakhunguyo.+ Ngati cheya cha pamalopo chasanduka choyera ndipo pakuoneka kuti m’pozama kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe aone nthendayo n’kugamula kuti munthuyo ndi wodetsedwa.