-
2 Mbiri 31:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Panalinso mndandanda wa mayina a ana a Aroni,+ ansembe, amene anali kukhala m’malo+ odyetserako ziweto kunja kwa mizinda yawo. M’mizinda yonseyo munali amuna amene anasankhidwa pochita kuwatchula mayina, kuti azipereka magawo a chakudya kwa mwamuna aliyense pakati pa ansembe ndiponso kwa Alevi onse amene anali pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo.
-