6Tsopano Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova.+ Anayamba kuchita zimenezi m’chaka cha 480 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo,+ m’mwezi wachiwiri+ wa Zivi.+ Ichi chinali chaka chachinayi+ cha ulamuliro wake monga mfumu ya Isiraeli.
3Kenako Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu paphiri la Moriya,+ pamalo amene Yehova anaonekera kwa Davide bambo ake.+ Anamanga nyumbayo pamalo amene Davide anali atakonza. Amenewa anali malo opunthira mbewu a Orinani+ Myebusi.