5 Komanso ziwiya zagolide ndi zasiliva+ za m’nyumba ya Mulungu, zimene Nebukadinezara+ anazichotsa m’kachisi yemwe anali ku Yerusalemu n’kuzipititsa ku Babulo, zibwezedwe kuti zipite kumalo ake, kukachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo zikaikidwe m’nyumba ya Mulungu.+