5 Koma maso+ a Mulungu wawo anali+ pa akulu a Ayuda, ndipo anthu aja sanawasiyitse ntchitoyo. Anadikira mpaka pamene analemba chikalata chokhudza nkhaniyo n’kuchitumiza kwa Dariyo, ndiponso mpaka pamene chikalata choyankha nkhani imeneyi chinabwera.