15 Ndiyeno ndinawasonkhanitsa pamtsinje+ umene umafika ku Ahava+ ndipo tinamanga msasa pamenepo n’kukhalapo masiku atatu kuti ndiwaonetsetse anthuwo+ ndi ansembe,+ koma sindinapezepo ana a Levi.+
21 Kenako ndinalamula kuti tisale kudya tili kumtsinje wa Ahava kuja, kuti tidzichepetse+ pamaso pa Mulungu wathu ndi kumupempha kuti atisonyeze njira yoyenera+ kwa ife, ana athu,+ ndi katundu wathu yense.