Genesis 3:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Kwa mkaziyo, Mulungu ananena kuti: “Ndidzawonjezera kuvutika kwako pamene uli ndi pakati.+ Pobereka ana udzamva zowawa.+ Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira.”+ Deuteronomo 22:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake,+ mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifera pamodzi. Mwamuna wogona ndi mkaziyo ndiponso mkaziyo azifera pamodzi.+ Motero uzichotsa oipawo mu Isiraeli.+ Yeremiya 31:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 “Koma pangano limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo.+ ‘Pangano langa limenelo analiphwanya+ ngakhale kuti ine ndinali mwamuna wawo,’+ watero Yehova.” Yoweli 1:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Lirani momvetsa chisoni ngati mmene amalirira namwali amene wavala chiguduli*+ polirira mwamuna amene anali kufuna kumukwatira. Mateyu 24:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa+ analowa m’chingalawa.+
16 Kwa mkaziyo, Mulungu ananena kuti: “Ndidzawonjezera kuvutika kwako pamene uli ndi pakati.+ Pobereka ana udzamva zowawa.+ Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira.”+
22 “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake,+ mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifera pamodzi. Mwamuna wogona ndi mkaziyo ndiponso mkaziyo azifera pamodzi.+ Motero uzichotsa oipawo mu Isiraeli.+
32 “Koma pangano limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo.+ ‘Pangano langa limenelo analiphwanya+ ngakhale kuti ine ndinali mwamuna wawo,’+ watero Yehova.”
8 Lirani momvetsa chisoni ngati mmene amalirira namwali amene wavala chiguduli*+ polirira mwamuna amene anali kufuna kumukwatira.
38 M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa+ analowa m’chingalawa.+