2 Mbiri 20:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 n’kunena kuti:+ “Inu Yehova Mulungu wa makolo athu,+ kodi si inu Mulungu wakumwamba?+ Kodi inu simukulamulira maufumu onse a mitundu ya anthu?+ Kodi m’dzanja lanu si muli mphamvu kotero kuti palibe amene angalimbane nanu?+ Danieli 4:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+ Machitidwe 11:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Chotero ngati Mulungu anapereka mphatso yaulere imodzimodziyo kwa iwo, monga mmenenso anachitira kwa ife amene tinakhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu,+ ine ndine ndani kuti ndiletse Mulungu?”+ Aroma 9:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Mwina unganene kwa ine kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani angatsutse chifuniro chake chimene chinanenedwa?”+
6 n’kunena kuti:+ “Inu Yehova Mulungu wa makolo athu,+ kodi si inu Mulungu wakumwamba?+ Kodi inu simukulamulira maufumu onse a mitundu ya anthu?+ Kodi m’dzanja lanu si muli mphamvu kotero kuti palibe amene angalimbane nanu?+
35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
17 Chotero ngati Mulungu anapereka mphatso yaulere imodzimodziyo kwa iwo, monga mmenenso anachitira kwa ife amene tinakhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu,+ ine ndine ndani kuti ndiletse Mulungu?”+
19 Mwina unganene kwa ine kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani angatsutse chifuniro chake chimene chinanenedwa?”+