Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pakuti sipadzalephera kukhala wosauka m’dziko lako.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti, ‘Uzikhala wowolowa manja kwa m’bale wako wovutika ndi wosauka m’dziko lanu.’+

  • Yobu 31:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ngati ndinkakaniza anthu onyozeka zopempha zawo,+

      Ndipo ngati ndinkachititsa chisoni maso a mkazi wamasiye,+

  • Salimo 112:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+

      צ [Tsa·dhehʹ]

      Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+

      ק [Qohph]

      Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+

  • Miyambo 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Munthu wonyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,+ koma wodala ndi munthu wokomera mtima anthu osautsika.+

  • Miyambo 19:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+

  • Mlaliki 11:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pereka gawo la zinthu zimene uli nazo kwa anthu 7, ngakhale 8,+ chifukwa sukudziwa tsoka limene lidzagwe padziko lapansi.+

  • 2 Timoteyo 1:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa iye anali kubwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa,+ ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena