1 Mbiri 5:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Pa nkhondoyo iwo anathandizidwa moti Ahagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa m’manja mwawo, popeza anapempha Mulungu kuti awathandize+ ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anam’khulupirira.+ Salimo 22:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Makolo athu anali kudalira inu.+Iwo anali kudalira inu ndipo munali kuwapulumutsa.+ Danieli 3:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ngati mungatiponyere m’ng’anjo yoyaka moto, Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa. Iye atipulumutsa m’ng’anjo yoyaka moto ndiponso m’manja mwanu mfumu.+ Danieli 6:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pamenepo mfumuyo inasangalala kwambiri+ ndipo inalamula kuti Danieli amutulutse m’dzenjemo. Danieli anatulutsidwadi m’dzenjelo ndipo sanavulale paliponse chifukwa anakhulupirira Mulungu wake.+
20 Pa nkhondoyo iwo anathandizidwa moti Ahagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa m’manja mwawo, popeza anapempha Mulungu kuti awathandize+ ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anam’khulupirira.+
17 Ngati mungatiponyere m’ng’anjo yoyaka moto, Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa. Iye atipulumutsa m’ng’anjo yoyaka moto ndiponso m’manja mwanu mfumu.+
23 Pamenepo mfumuyo inasangalala kwambiri+ ndipo inalamula kuti Danieli amutulutse m’dzenjemo. Danieli anatulutsidwadi m’dzenjelo ndipo sanavulale paliponse chifukwa anakhulupirira Mulungu wake.+