Salimo 3:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndidzafuulira Yehova mokweza,Ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.+ [Seʹlah.] Salimo 145:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.+Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi,+ Yesaya 30:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Anthu a ku Ziyoni+ akadzabwerera n’kukakhala ku Yerusalemu,+ iwe sudzaliranso.+ Mosakayikira, iye adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako. Akadzangomva kulira kwakoko, iye adzakuyankha.+ Aheberi 5:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha,+ kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula+ komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.+
19 Anthu a ku Ziyoni+ akadzabwerera n’kukakhala ku Yerusalemu,+ iwe sudzaliranso.+ Mosakayikira, iye adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako. Akadzangomva kulira kwakoko, iye adzakuyankha.+
7 Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha,+ kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula+ komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.+